Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 223
Paphata pa Chichewa
Lemeretsa: Kupatsa wina chuma.
Chitsanzo: Geniyi indilemeretsa.
Lenguka (lengula): Kufuna kugwa kapena kukomoka, ku-
kupangitsa chizungulire, kufooka.
Chitsanzo: Nsima ndinadya ija yandilengula.
Lephethe: Kunyowa.
Chitsanzo: Zovala zanga zonse ndinazipeza zili lephethe!
Lerera mwana pachinena (pachilolo): Kulera mwana mo-
musasatitsa, momupusitsa.
Chitsanzo: Ngati amakulererani pachinena (pachilolo)
n’kwanu komweko, kuno ayi!
Lidzakhalako dothi: Idzakhalapo ndewu.
Chitsanzo: Akadzakamba zopusa lidzakhalako dothi.
Likasa:
(a) Pepala lomwe ana ena amalembapo mayankho a ma-
funso n’cholinga choti akaonere mayeso.
Chitsanzo: Anamugwira ndi likasa.
(b) Bokosi lapadera lomwe limatchulidwa m’Baibulo.
Chitsanzo: Bezaleli ndi amene anapanga Likasa.
Likita mowa: Kuledzera, kumwa mowa wambiri.
Chitsanzo: Lero ndiye ndiulikita mowa.
Lima pamsana: Kuchenjeretsa munthu, kuchitira
nkhanza.
Chitsanzo: Timagwira ntchito mokhulupirika, koma
mabwana anthu amangotilima pamsana.
Limba chiwindi: Limba mtima.
Chitsanzo: Kupha njoka kumafuna munthu wolimba
chiwindi.
Limba mtima:
(a) Kupanda mantha.
Chitsanzo: Kuchita bizinezi ya makala kukumafuna
munthu wolimba mtima.
222