Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 222
Paphata pa Chichewa
Laponda diwa: Kuchita mwayi.
Chitsanzo: Laponda diwa, ntchito ikumasowa masiku
ano!
Laponda lamphawi: Kuchita mwayi.
Chitsanzo: Atandiitanira nsimayo, ndinangoti laponda
lamphawi!
Lasa:
(a) Kunena mfundo yomveka.
Chitsanzo: Apo ndiye mwalasatu, mfundo koma imeneyo.
(b) Kunena mawu opweteka.
Chitsanzo: Mawu mwayankhulawo andilansa mumtima.
(c) Kupereka mimba.
Chitsanzo: (1) Mwamuna akapereka mimba timati walasa.
(2) Mnyamata ankamuderera ujatu walasa.
Lawira:
(a) Kutsanzika.
Chitsanzo: Ndikupita kukawalawira achimwene kuseriku.
(b) Kulawa chinthu m’malo mwa munthu wina.
Chitsanzo: Bwerani tikulawireni ngati zili ndi mchere.
(c) Kunyamuka m’mawa kwambiri.
Chitsanzo: Mawa ndilawira kwambiri.
Ledzera ndi mphamvu: Chita nkhanza.
Chitsanzo: Wolamulira akaledzera ndi mphamvu ama-
yamba kugwira anthu n’kumakadyetsera ng’ona.
Lemba: Pusitsa, dyetsa njomba. Mawuwa amachokera ku
zimene wosewera mpira amachita akamadyetsa njomba
anzake.
Chitsanzo: Musadzampatsenso ndalama zanu, adzaku-
lembani.
Lembam’madzi: Lephera.
Chitsanzo: Walembam’madzi, amaganiza angandipusitse.
Lemberana chimfine: Kumana onse a pachibale.
Chitsanzo: Anthu onse a pamudzipa akulemberana
chimfine lero.
221