Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 221

Paphata pa Chichewa Labadira (labada): Kumvera, kutsatira. Chitsanzo: (1) Sakulabada kuti mwana wawo akuvutika. (2) Agogo salabadira za munthu. Lakalaka: Kufunitsitsa. Chitsanzo: Ndikulakalaka nditadya dothi. Lalamuka: Kulalata, kukalipa. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani mumalalamuka dzulo lija? Lalata: Kunena chipongwe mokweza. Chitsanzo: Anabwera kudzandilalatira. Lambalala: (a) Nena nkhani mozungulira. Chitsanzo: Kuyankha kwake amachita molambalala. (b) Dutsa mozungulira. Chitsanzo: Mnzako akapunthwa n’kuthyoka mwendo, iwe umalambalala m’mbalimo. Lambula njira: Kukonzekera, kuyambirira kuchita chinachake. Chitsanzo: John Chilembwe ndi amene analambula njira ya ufulu m’Malawi muno. Lamwa (Lamwira): Kupusa. Chitsanzo: (1) Sindifuna mwana wolamwa chonchi. (2) Ku- lamwira sikusiyana ndi uchitsiru. Landitsa ndewu: Kuleletsa ndewu, kusiyitsa anthu kumenyana. Chitsanzo: Akulanditsa ndewu kumtundaku. Landula: Kumukana pagulu, kumuthamangitsa. Chitsanzo: Achimwene awo analandula akazi awo. Langiza kuphazi: Kuthawa. Chitsanzo: Mbalayo itaona kuti anthu aiona, inalangiza kuphazi. Lapitsa: Kumenya munthu kwambiri. Chitsanzo: Amumenya molapitsa. 220