Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 220
Paphata pa Chichewa
anzanu onse anakwatiwa ndi pantchafu.
Kwawo kapande: Zipitani kwanu.
Chitsanzo: Kwada tsopano, kwawo kapande.
Kwaya wausiku (eko wausiku): Kupatsa munthu
pang’ono.
Chitsanzo: Ukamapereka chinthu kwa munthu
osamachita kwaya wausiku ngati anakupempha.
Kwayauwotche: Matenda opatsirana pogonana.
Chitsanzo: (1) Mwana wa Anamasina anatenga kwayau-
wotche. (2) Ukamangoti maso m’mwamba anthu akupatsa
kwayauwotche.
Kwenya: Gwira malaya a munthu pomuopseza.
Chitsanzo: Anamukwenya mpaka lamba kuduka.
Kwera chitunda: Mawuwa amanenedwa munthu ak-
amakumana ndi mavuto.
Chitsanzo: Anzanu ajatu akukwera chitunda.
Kwera pachulu: Kulalata, kutukwana.
Chitsanzo: Akapanda kubweretsa ndimukwerera pachulu.
Kwera paudindo: Kupatsidwa udindo waukulu.
Chitsanzo: Anthu amene amakwera paudindo amakhala
olimbikira.
Kweza changa m’mwamba: Pulumutsa.
Chitsanzo: Ntchito anatiuza kuti tikagwireyo inali yovuta.
Mwamwayi kapitawo anandiuza kuti anthu akwanira moti
anakweza changa m’mwamba.
Kwidzinga: Mawu okokomeza onena za munthu amene
wamangidwa atapalamula.
Chitsanzo: Wakubayo anamukwidzinga ndi unyolo.
Kwingwinyala: Chita manyazi.
Chitsanzo: (1) Atangomuseka, nthawi yomweyo
anakwingwinyala. (2) Bodza lako likaonekera
umangokwingwinyala.
219