Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 219
Paphata pa Chichewa
Kuzwetetsa mutu: Kusokoneza mutu.
Chitsanzo: Mavutowa ndi ozwetetsa mutu.
Kwadzaoneni: Kwambiri.
Chitsanzo: Mvula ikugwa mwadzaoneni.
Kwagwa chiuta: Kwachitika maliro.
Chitsanzo: Kumtundaku kwagwa chiuta.
Kwakwatuke: Munthu wasauka.
Chitsanzo: (1) Ngati ukufuna chikondi kwatiwa ndi kwak-
watuke, ngati ukufuna ndalama, kwatiwa ndi khumucha.
(2) Amene uja ndi kwakwatuke wotheratu, adzalemera
akadzafa.
Kwalimbauta: Munthu wopanda mfundo kapena
maganizo ake enieni.
Chitsanzo: Mukutaya nthawi ndi kwalimbauta uja?
Kwamnanu: Kwambiri.
Chitsanzo: Akukumana ndi mavuto amnanu.
Kwapatira: Kupana chinthu ndi mkono m’khwapa.
Chitsanzo: Akwapatira chikwama.
Kwapula nyimbo/nkhani: Kuimba nyimbo mwaluso zedi,
kukamba nkhani mwaluso zedi.
Chitsanzo: (1) Chibadula ankakwapula nyimbo. (2) Mwa-
nayu waikwapula nkhani.
Kwapula: Menya mwankhanza.
Chitsanzo: Mukamuputa akukwapulani.
(b) Kumenya pogwiritsa ntchito chikwapu.
Chitsanzo: Mwana wosamvera amafunika kumukwapula.
Kwatiwa n’kumbuyo komwe: Kukwatiwa ndi munthu
wolemera.
Chitsanzo: Inutu ndiye munakwatiwa ndi kumbuyo kom-
we, anzanu onse anakwatiwa m’pantchafu.
Kwatiwa ndi pantchafu: Kukwatiwa ndi munthu wosau-
ka.
Chitsanzo: Inutu ndiye munakwatiwa n’kumbuyo komwe,
218