Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 218
Paphata pa Chichewa
Kuzisiya: Kulephera, kugonja.
Chitsanzo: Osewera amatama aja azisiya.
Kuzonda:
(a) Kudana ndi munthu, kuzondana ndi kusaonana
bwino.
Chitsanzo: Anthu amenewa amandizonda.
(b) Kukaona anthu.
Chitsanzo: (1) Amene anabwera kudzatizonda ndi am-
alume awo. (2) Ndinapita kukazonda matenda.
Kuzondotsa: Kulozetsa chinthu pansi.
Chitsanzo: (1) Mabukuwa mwawaika mozondoka. (2)
Mwazondotsa, mituyi izikhala m’mwamba.
Kuzuka:
(a) Munthu wamtali komanso wamkulu thupi.
Chitsanzo: Mtsikana wake ndi wozuka.
(b) Kuchoka mumthaka.
Chitsanzo: Chinakwa sichichedwa kuzuka.
Kuzula minga ya pamsana: Thandiza kwambiri.
Chitsanzo: Amenewa ndi amene anandizula minga ya
pamsana zitandivuta chaka chatha.
Kuzuna: Kukoma kwambiri, kusangalatsa, kutsekemera
kwambiri.
Chitsanzo: (1) Nkhani mwalembayi ndi yozuna. (2) Uchi
umazuna.
Kuzungulira mutu: Kuchita misala, kusaganiza bwino.
Chitsanzo: (1) Kodi ndiwe wozungulira mutu eti? (2) Ana
awo onse ndi ozungulira mitu.
Kuzunguza: Kuvutitsa, kuvuta kwa chinthu.
Chitsanzo: (1) Mwanayu ndi wozunguza. (2) Samuyi ndi
yozunguza.
Kuzunguzika: Kusokonezeka.
Chitsanzo: Ngoziyo itachitika, bamboyo anazunguzika
maganizo.
217