Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 217
Paphata pa Chichewa
(b) Kukhazikika.
Chitsanzo: Sitifuna kuti alendo azizika mizu pakhomo
pano
Kuzilala: Kufooka, kuzima.
Chitsanzo: (1) Nkhosa zambiri za tchalitchi ichi zinazilala.
(2) Moto uja wazilala.
Kuzimiratu: Kugoneratu.
Chitsanzo: Anabwera usiku kwambiri moti ndinali
nditazimiratu.
Kuzimiririka: Kusaonekanso, kutsenjira.
Chitsanzo: (1) Pamene ndimazindikira kuti wandibera
n’kuti munthuyo atazimiririka. (2) Ndinamuona akubwera
koma kenako anangozimiririka.
Kuzimuka: Kumvetsera Mawu a Mulungu kapena nyimbo
zauzimu.
Chitsanzo: Tipite kutchalitchi tikazimuke.
Kuzingwa kwa Kalulu kukapsa: Kutanganidwa kosowa
nako chochita.
Chitsanzo: Kumenekutu ndiye kuzingwa kwa kwalulu
kukapsa.
Kuzingwa: Kusokonezeka, kusowa pogwira.
Chitsanzo: (1) Galu wangayu ndi amene anamuzigwitsa
kalulu uja. (2) Ukazigwa vuto lililonse limakhala ngati
phiri.
Kuzipulumutsa zibakera: Kumenya munthu ndi
zibakera.
Chitsanzo: Anthu achibwibwi sachedwa kuzipulumutsa
zibakera ukamawauza zachihatahata.
Kuzisaka: Kufufuza ndalama.
Chitsanzo: (1) Atsikana a masiku ano ndi ozisaka. (2)
Kungodikira kapena kuyenda ulendo popanda kanthu,
kulephera.
216