Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 216

Paphata pa Chichewa (b) Kumwalira. Chitsanzo: (1) Anthu akuyoyoka ndi matenda. (2) Edzi ikuyoyola anthu. Kuyoyoka: (a) Kugwa pansi. Chitsanzo: Nandolo yense wayoyoka. (b) Kupha. Chitsanzo: Masiku ano matenda akuyoyola anthu osaneneka. Kuzaza (kuzazira): Kukalipa. Chitsanzo: Akakupezani akuzazirani. Kuzemberera: Kuchita zinthu mwakabisira ukufuna munthu wina kapena chinachake. Chitsanzo: Anyamatawa akuzemberera atsikana anu aja. Kuzengereza: Kunyalanyaza, kusafuna kuchitiratu chinthu. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani mumazengereza kubwera, ndinakusungirani nsimatu? Kuzerezeka: Kusiya kuganiza bwino. Chitsanzo: Bambo aja ndi ozerezeka, zoona kumakolopa m’nyumba akazi awo akugona. Kuzezeduka: Kuchenjeretsa. Chitsanzo: Mwanayu ndi wozezeduka. Kuzichunachuna: Kuzikongoletsa, kuzikonzakonza. Chitsanzo: Pa tsiku la chikondwererocho, azimayi onse anazichunachuna. Kuzigwa: Kusowa chochita. Chitsanzo: Ukazigwa, ngakhale khala losayaka limatha kukuotcha. Kuzika: (a) Kulowetsa pansi. Chitsanzo: Zikani mtengowu apa! 215