Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 214

Paphata pa Chichewa (b) Kugulidwa ndi anthu ambiri. Chitsanzo: Chimangachi chikuyenda malonda. Kuyenda modzithinula: Kuyenda monyada. Chitsanzo: Akabwera kumene kutauni amayenda modzithinula. Kuyenda mwamdidi: Kuyenda mopanda choopa. Chitsanzo: Akakatamuka amayenda mwamdidi. Kuyenda n’kuvina: Sungadziwe kuti mawa ukapezeka kuti, kuyenda sikudziwika. Chitsanzo: (1) Ukakumana ndi munthu, osamamuchitira chipongwe chifukwa kuyenda n’kuvina. (2) Mwina tidza- kumananso, kuyenda n’kuvina. Kuyenda ndawala: Kuyenda mofulumira. Chitsanzo: Tiyeni tiziyenda ndawala tingachedwe. Kuyenda ndi dziko (kuthamanga ndi dziko): Kuchita zonse zimene zikuchitika m’dzikoli, kuchita makhalidwe oipa. Chitsanzo: Amayenda ndi dziko, lero lamutembenukira. Kuyenda ndi mdidi: Kuyenda mopanda mantha. Chitsanzo: Akakhala nazo ndalama amayenda ndi m’didi. Kuyenda pakhomo pali pululu: Kuyenda osatseka zipi, lisani. Chitsanzo: Abwana athu amayenda pakhomo pali pululu. Kuyenda pamlatho waphesi: kuyaluka chifukwa cha khalidwe loipa. Chitsanzo: Akuyenda pamlatho waphesi chifukwa cha khalidwe lake lachisembwere. Kuyenda punzipunzi: Kuyenda modzikoka, kuyenda ngati ukufuna kugwa, kudzandira. Chitsanzo: Agogo anabwera kuno akuyenda punzipunzi chifukwa cha ukalamba. 213