Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 211
Paphata pa Chichewa
Kuyamika wamoto: Kuyamikira mofulumira usanaone
khalidwe lenileni.
Chitsanzo: Aliyense ankanena zabwino za munthu
ameneyu, koma ankayamika wamoto.
Kuyang’ana ndi diso loipa: Kuyang’ana munthu
momuzonda, mosonyeza kuti umadana naye.
Chitsanzo: Masiku ano akumandiyang’ana ndi diso loipa.
Kuyangalayangala: Kuyendayenda.
Chitsanzo: Sagwira ntchito, amangokhalira
kuyangalayangala m’taunimu.
Kuyankha mosisitika: Kuyankha mosatsimikiza,
kuyankha motsika kwambiri.
Chitsanzo: Atawafunsa ngati zinali zoona anayankha mo-
sisitika.
Kuyankha mwala: Kuyankha mwano.
Chitsanzo: (1) Mayiyo anamupeza akusetekera m’manja.
Atamuuza kuti akuchitawo ndi uve, anamuyankha mwa-
la. (2) N’chifukwa chiyani masiku ano ukumangondi-
yankha mwala?
Kuyankha ziphaliwali: Kuyankha mwano.
Chitsanzo: Nditamufunsa amangondiyankha ziphaliwali.
Kuyankhula chidamula: Kuyankhula mongodula,
zosamveka.
Chitsanzo: Ndikakumana nawo akumangoyankhula
chidamula.
Kuyankhula Chigiriki: Kuyankhula zosamveka.
Chitsanzo: Enawatu amaona ngati mukuyankhula
Chigiriki.
Kuyankhula chikapaya: Kuyankhula zosamveka,
mozungulira.
Chitsanzo: Ukamafunsira sumafunika kumayankhula
chikapaya.
210