Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 210
Paphata pa Chichewa
Kuyabwa:
(a) Kunyong’onyeka kapena kusafuna kukhala pansi.
Chitsanzo: Bibida ndi amene amawalowa m’thumba, moti
akapeza ndalama pakhomo pano pamawayabwa.
(b) Kuvutitsa.
Chitsanzo: Abwera tsopano, akufuna atiyabwe!
Kuyabwidwa ndi chitedze: Kupalamula.
Chitsanzo: Samadziwa kuti akuputa mavu nkhomola moti
chitedze chinamuyabwa.
kuyaka ndi nkwiyo: Kupsa mtima kwambiri.
Chitsanzo: Ndinawapeza akuyaka ndi nkwiyo.
Kuyaka: Kuledzera.
Chitsanzo: Ndinakumana nawo atayakiratu.
Kuyala masamba auma: Dikirira nthawi yaitali.
Chitsanzo: Anakhala pamenepo mpaka masamba auma.
Kuyala nkhani yonse: Kufotokoza zonse mwatsatanetsa-
tane.
Chitsanzo: Bwerani ndikuyalireni nkhani yonse.
Kuyala udzu pamimba: Kupusitsa munthu.
Chitsanzo: Akungofuna kukuyala udzu pamimba.
Kuyaluka: Kuchita manyazi kapena kupusa.
Chitsanzo: (1) Mukamangouza aliyense nkhani imeneyi
muwayalutsa amuna anu aja. (2) Mukamalimbana nawo
akuyalutsani. (3) Mukagwidwa muyaluka.
Kuyalutsa: Kuulula zinthu zachinsinsi, kunyoza kothera-
tu.
Chitsanzo: (1) Zochita za mayi aja zimayalutsa amuna
awo. (2) Koma ndiye wayalukatu!
Kuyambukira: Kukukhudza, kuyamba kuchita zinazake.
Chitsanzo: (1) Makhalidwe oipawa akuyambukirani. (2) Zo-
chita za makolo zimayambukira ana.
209