Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 21

Paphata pa Chichewa Bwezera phala kum’kobwe: Kusathokoza, kupanda pabwino. Chitsanzo: Zimene mukuchitazitu sizikuthandizani. Simukudziwa kuti mukubwezera phala kum’kobwe? Bwira dothi: (a) Kulephera. Chitsanzo: Tikamamuuza kuti azilimbikira amatiyesa ankhanza, lero si izi wabwira dothi! (b) Kuchimwa. Chitsanzo: Munthu wachitsanzo chabwino uja anabwira dothi mumpingo. (c) Kugwa pansi. Chitsanzo: Amathamanga ndipo wagwa n’kubwira dothi. Bwitibwiti: Zonona, za mafuta ambiri. Chitsanzo: Ndiwo zake zinali za bwitibwiti. Bwitikiza: Kudzoza (kupaka) mafuta ambiri kapena zinthu zina. Chitsanzo: Ali ndi khungu ngati la ng’ona moti kuti awaleko amafunika kudzibwitikiza m’mafuta. Bwize: Munthu wakuba. Chitsanzo: Samalani, kwabwera bwize. Bzala chinangwa: Kumwalira. Mawuwa anabwera chifukwa munthu akabzala chinagwa, osati mtengo, chinangwacho chimangowola. Chitsanzo: Mkhalakale zonse zidabzala chinangwa. Bzala ufa: Kunama. Chitsanzo: (1) Ndinachita kudziwiratu kuti akubzala ufa. (2) Umaganiza kuti ukabzala ufa ife sitidziwa. 20