Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 209

Paphata pa Chichewa Kuwolowa manja: Kukhala opatsa. Chitsanzo: Bambowa ndi owolowa manja. Kuwolowa: Kufewa. Chitsanzo: Ndaviika mpunga kuti uwolowe. Kuwongokera: Kuchira. Chitsanzo: Bola panopa odwala aja akuwongokera. Kuwongola miyendo: Kupita koyenda. Chitsanzo: Apita kukaongola miyendo. Kuwongola miyendo: Kupita koyenda. Chitsanzo: Ndikupita kumtundaku kukawongola miyendo. Kuwonjola: (a) Kuthandiza. Chitsanzo: Ndikulalakala wina atabwera kuti adzandiwon- jole pamavutowa. (b) Kuchotsa nyama pansampha. Chitsanzo: Ndikupita kukawonjola nyama kumisampha yanga. Kuwononga ndalama: Kugwiritsa ntchito ndalama mosasamala. Chitsanzo: Mkazi ameneyu amawononga ndalama osati pang’ono. Kuwotcha: Kulephera kuchita chimene umafuna, kungowononga nthawi osapeza zimene umafuna. Angatanthauzenso kungodikira kapena kuyenda ulendo popanda kanthu, kulephera.. Chitsanzo: (1) Ndikanadziwa sindikanabwera, ndangowotcha ndalama zanga. (2) Amene anapita dzulo wangowotcha. Kuwowoza: Kukuwiza munthu. Chitsanzo: Mwana wolephera mayesoyo anamuwowoza mpaka kulira. 208