Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 208

Paphata pa Chichewa (b) Kutututsa gule ngati mmene amachitira Achewa. Chitsanzo: Zikuoneka kuti zilombo zawedza. Kuwenga: (a) Kudwalitsa matenda enaake monga chipere. Chitsanzo: Nsomba ya bombe imandiwenga. (b) Kudula zikhadabo ndi lumo. Chitsanzo: Amene sanawenge zala saadya ndi ine! Kuwerengera mbewa ndi michira yomwe: Kuwerengera zinthu zoti kulibe. Chitsanzo: Kodi nafenso timangowerengera ndi michira yomwe? Kuwerengera: Kudalira pomwepo. Chitsanzo: Nanenso ndikuwerengera pomwepa. Kuweta ana: Kulela ana mowasasatitsa. Chitsanzo: Kodi ana anuwa mumawaweta bwanji? Kuweyeseka: (a) Kutoperetu. Chitsanzo: Koma ndiye ndaweyeseka ndi ulendowu. (b) Kutheratu, kugwa. Chitsanzo: Nyumba yawo yaweyeseka ndi mphepo. Kuwezuka: (a) Kuyamba kuphya. Chitsanzo: Mango ayamba kuwezuka. (b) Kusintha mtundu, kuyera. Chitsanzo: Akumasamba kawirikawiri kuti awezuke. (c) Kukhala woyera. Chitsanzo: Ana awo onse ndi owezuka. Kuwiringula: Kudandaula, kunyinyirika. Chitsanzo: Anthu onse omwe ankawiringula anawapirikitsa. Kuwiringula: Kukana mlandu. Chitsanzo: Atamufunsa ngati anali wolakwa, anayamba kuwiringula. 207