Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 207

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Akagula kanyama amafuna kumatiwalira ndipo amatulutsa mbaula n’kumaphikira pabwalo. (2) Kuoneka bwino. Chitsanzo: Anzathu ndiye mukuwalatu! Kuwapezerera: Kuwapeza akuchita zinthu zoipa mwadzidzidzi. Chitsanzo: Anawapezerera akuba ndiwo mumphika. Kuwawasa: Kufika povuta kwambiri. Chitsanzo: Kuntchitoku kwawawasa. Kuwawitsa moyo (kukuwawa): Kukwiya kwambiri. Chitsanzo: (1) Zimene mwachitazi zawawitsa moyo wanga. (2) Mwachitazi zandiwawa. Kuwayawaya: Kuyendayenda. Chitsanzo: Akungowayawaya m’taunimu. Kuwaza mchenga m’maso: Kupusitsa. Chitsanzo: Akabwera, musalole kuti akuwazeni mchenga m’maso. Kuwaza: (a) Kuchita zinthu zosangalatsa kapena kukhala wosangalatsa kwambiri. Chitsanzo: (1) Nkhani imene amafotokoza yandiwaza kwabasi. (2) Amwene inuyo mumandiwaza kwambiri. (b) Kuswa chipika ndi nkhwangwa kapena chinthu china. Chitsanzo: Awaza nkhuni zambirimbiri. Kuwedza: (a) Kusinza. Nthawi zambiri munthu akamasinza amagwetsa mutu, ndiye akadzidzimuka amaudzutsa. Zimenezi n’zofanana ndi zimene zimachitika munthu akamawedza. Chitsanzo: Chifukwa cha kutentha, anthu ambiri akumawedza. 206