Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 206

Paphata pa Chichewa Kuvala ngati akupita kubafa: Kuvala zovala zosayenera kuvala pagulu. Chitsanzo: Kodi abambo amene aja amangoyayang’ana akazi awo aja akumavala ngati akupita kubafa? Kuvinidwa: Mawuwa anabwera kuchokera ku mwambo umene umachitika m’zikhalidwe zambiri woti mwana akakula amamupititsa ku chinamwali kuti akamuphunz- itse zoyenera ndi zosayenera kuchita. Mwana aka- malephera kusonyeza khalidwe labwino amangoti ndi wosavinidwa. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani umachita mwano, kusav- inidwa eti? Kuvula munthu: Kukulalatira, kukutukwana. Chitsanzo: Kaya ayambana nawo chiyani? Anawavula anzawo palaini ngati pamene paja. Kuvulalira mkati: (a) Kutenga matenda opatsirana pogonana. Chitsanzo: Mayiyu anavulalira mkati. (b) Kumva kupweteka mumtima. Chitsanzo: Sindikufuna kuonetsera, ndikungovulalira mkati. (c) Kuvulala mkati mwa thupi utachita ngozi. Chitsanzo: Atachita ngoziyo anavulalira mkati moti sipanatenge nthawi anamwalira. Kuvulira kachipewa: Kupereka ulemu. Chitsanzo: Mwayenda ulendo wonsewu wapansi? Takuvulirani kachipewa. Kuvundula: Kusokoneza, kupukusa. Chitsanzo: Ndani amene wavundula madziwa. Kuvunganyiza: Kusakanizasakaniza. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani wavunganyiza zovalazi? Kuwala: (a) Kuyerekedwa, kudzitama. 205