Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 205

Paphata pa Chichewa Kuuma khosi: Kusamva. Chitsanzo: Munthu wake ndi wouma khosi, kumulangiza samamva. Kuuma mtima: Kupanda chisoni. Chitsanzo: (1) Andiumira mtima ndithu mpaka osan- dipatsa. (2) Bambowa ndi wouma mtima. Kuunguzaunguza: (a) Kuganizaganiza. Chitsanzo: Ataunguzaunguza, anaona kuti si bwino kuyankha nthawi yomweyo. (b) Kuyang’anayang’ana Chitsanzo: Nditaunguzaunguza, sindinawaone. Kuunikira: Kuthandiza munthu nzeru, kudziwitsa. Chitsanzo: Sindinabwere kudzakuimbani mlandu, ndimangofuna kukuunikirani. Kuunjika: Kubiba, kunyera. Tanthauzo lake lenileni ndi kuika zinthu zambiri pamalo amodzi. Chitsanzo: Ndani waunjika m’chimangamu? Kuupeza mtima: Osapupuluma, kumadekha. Chitsanzo: (1) Achimwene, kumaupeza mtima, mudzapeza zanu m’tsogolo. (2) Kuti upeze zabwino umafunika kuupe- za mtima. Kuusumana: Kumva bwino, kusangalala. Chitsanzo: Ndinawapeza akuusumana pabala penapake. Kuutha: Kudziwa kusewera mpira. Chitsanzo: Mwanayu amautha mpira. Kuutsa chenjerere: Kuchititsa kuti wina akwiye kwambiri. Chitsanzo: Mwana ameneyu wautsa chenjerere. Kuutunga mowa: Kumwa kwambiri mowa, kuledzera. Chitsanzo: Akautunga mowa amavuta kwambiri. 204