Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 204
Paphata pa Chichewa
Kutula pansi: Kusiya udindo.
Chitsanzo: Pulezidenti wadziko la Malawi watula pansi
udindo wake.
Kutumbiza: Kubereka mwana, mwana wina asanakule.
Chitsanzo: Sindimafuna kudzatumbiza pamoyo wanga.
Kutumbwa: Kuyerekedwa, kuchita matama.
Chitsanzo: Anthu ena amayankhula motumbwa pamaliro
ngati sadzafa.
Kutupikana: Kutupa chifukwa cha matenda kapena
kusowa zakudya m’thupi.
Chitsanzo: Mwanayu akutupikana.
Kutuwa: Kuvutika kwambiri.
Chitsanzo: Chaka chino tituwa koopsa.
Kutuzula maso: Kutulutsa diso lonse pamtunda.
Chitsanzo: Akalusa amandiyang’ana atatuzula maso.
Kuudziwa mpira: Kudziwa kusewera mpira.
Chitsanzo: Mwanayu amaudziwa mpira.
Kuugwira mtima: Kudziletsa kuti usayankhule kapena
kuchita chinthu choipa.
Chitsanzo: Achimwene anu aja amafunika munthu woug-
wira mtima.
Kuuluka (kutamba): Zokhudzana ndi ufiti. Mawuwa an-
thu ena amawagwiritsa ntchito poganiza kuti munthu
akhoza kuuluka usiku pogwiritsa ntchito tsache kapena
lichero. Ndi zikhulupiriro chabe basi chifukwa palibe
anaonapo zikuchitika.
Chitsanzo: Nawonso anzanuwa akukhala ngati amauluka
bwanji?
Kuuluka: Kuthamanga kwambiri.
Chitsanzo: Mwabwerako nthawi yomweyi, koma ndiye
mwaulukatu!
203