Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 202
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Wodwalayo anayamba kutsalima ife tili pom-
wepo.
Kutsangula misozi: Kutonthoza ena, kupukuta misozi.
Chitsanzo: Amene anabwera kudzatitsangula misozi ndi
achimwene basi.
Kutseguka m’maso: Kuzindikira.
Chitsanzo: (1) Apatu ndiye mwanditsegula m’maso, sindi-
madziwa kanthu. (2) Zimene a zaumoyo atiuza zatitsegula
m’maso.
Kutseguka m’mutu: Kuzindikira kapena kumvetsa zi-
nazake.
Chitsanzo: (1) Apatu ndiye ndatseguka m’mutu, sindi-
madziwa kuti malambe ndi ofunika chonchi! (2) Ma-
phunziro amenewa anditsegula m’mutu.
Kutsegula pakamwa: Kuyankhula.
Chitsanzo: Amaonekadi waulemu, koma akangotsegula
pakamwa mpamene ndinadziwa kuti ndi khuluku.
Kutsenjira: Kusowa osaonekanso, kuzimiririka, kubisika.
Chitsanzo: (1) Anaima pakantinipo kwa nthawi yaitali, ko-
ma kenako anangotsenjira. (2) Ndinyamuka dzuwa lika-
tsenjira.
Kutsika kwa mvula: Kugwa kwambiri kwa mvula.
Chitsanzo: Koma ndiye chaka chino mvula yatsikatu.
Kutsikira kulichete: Kumanda.
Chitsanzo: Ana awo onse anatsikira kulichete.
Kutsimphina: Kuyenda movutikira.
Chitsanzo: Mwanayu watani akuyenda motsimphina?
Kutsina khutu: Kuululira munthu chinsinsi.
Chitsanzo: Ndinawakokera pambali kuti ndiwatsine
khutu.
Kutsinira mafulufute kuuna: Kutsekereza mwayi.
Chitsanzo: Ukanalimbikira akanakupatsanso, koma
watsinira mafulufute kuuna.
201