Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 201

Paphata pa Chichewa (b) Kuwira. Chitsanzo: Ndiwo zija zayamba kutokota. Kutokota: Kulalata, kuvuta. Tanthauzo lake lenileni ndi kuwira. Chitsanzo: Abwanawa amatokota koopsa. Kutokotera: Kulalata, kuvuta. Chitsanzo: Ndinawapeza akuwatokotera. Kutola chikwama: Kulemera. Chitsanzo: Anzanu aja anatola chikwama. Kutola chithunzi: Kujambula munthu ndi kamera, foni kapena tabuleti. Chitsanzo: Tikufuna tikatoletse zinthunzi. Kutola nkhwangwa ndi mpini womwe: Kuchita mwayi waukulu. Chitsanzo: Anzathutu mwatola nkhwangwa ndi mpini womwe. Mpaka kulandira mbewu ndi feteleza yemwe! Kutolera: Kulandira ndalama zako. Chitsanzo: Ndikupatsani ndikatolera. Kutolera: Kupeza ndalama. Chitsanzo: Mundidikire mwezi ukatha kuti nditolere kaye. Kutolerana: Kumvana, kugwirizana. Chitsanzo: Anthuwa amatolerana. Kutong’ola: (a) Kuchotsa chimanga kuchitsononkho. Chitsanzo: Mutong’ole chimangachi. (b) Kutuzula maso. Chitsanzo: Akalusa amandiyang’ana atatong’ola maso. Kutsala mafupa okhaokha: Kuonda kwambiri. Chitsanzo: Mutawaona simungawadziwe, angotsala mafupa okhaokha. Kutsalima: Kuthatha, kuphupha mosonyeza kuti moyo ukuchoka. 200