Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 20

Paphata pa Chichewa Buothaotha moto (kuotha moto): Palamula. Chitsanzo: Amene uja auotha moto lero. Bwalula uzimba: Kuyamba bwino uzimba mwa kupha nyama. Chitsanzo: Ndikapita kosaka ndi awa timabwalula uzimba. Bwanyula pakamwa: Kum’menya pakamwa. Chitsanzo: Anamubwanyula pakamwa chifukwa amayankhula zopanda pake. Bwatabwata phulu: Yankhula mwachibwana. Chitsanzo: Ukayankhulanso za bwatabwata phulu, akuphofomola. Bwenzi lamphasa: Munthu wodwaladwala. Chitsanzo: Mwana wamasiye uja wasanduka bwenzi lamphasa. Bwerera kumanda: Kuchira utadwala mwakayakaya. Chitsanzo: Abwerera kumanda awa, moyo timaonera pakhosi. Bwerera lili pululu: Kuchira utadwala mwakayakaya. Chitsanzo: Ndikadafa ine, ndabwerera lili pululu. Bwerera lokumbakumba: Kuchira utadwala mwakayakaya. Chitsanzo: Anadwala zedi moti abwerera lokumbakumba. Bwererana: Mawuwa amanenedwa ngati munthu banja linatha ndiye anthuwo ayambanso kukhala limodzi. Chitsanzo: (1) Achemwa akuganiza zobwererana ndi amuna awo. (2) Anthu anasudzulana aja abwererana. 19