Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 199

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Anzake amuthetsa makani. Kuthetsa mankhalu: Kudabwitsa munthu, kukhaulitsa munthu. Chitsanzo: (1) Sindinaonepo munthu wokakamira chonchi moti wandithetsa mankhalu. (2) Anamanga sukulu mothetsa mankhalu. Kuthetsa nzeru (kuthedwa nzeru): Kusowa chochita. Chitsanzo: Mavutowa andithetsa nzeru. Kuthiga: Kukhuta bwino, kukwanira bwino. Chitsanzo: Amalemba Chichewa chothiga ndi nsinjiro za chiyankhulo. Kuthima: (a) Kuledzera. Chitsanzo: Ndinakumana nawo atathima. (b) Kubaizika. Chitsanzo: Pepani ndinathima, mumati chiyani? (c) Kumwalira. Chitsanzo: Munthu uja wathima. Kuthimba pakhosi: Kuima pakhosi. Chitsanzo: Mbatata yamuthimba pakhosi. Kuthimbirira: (a) Kuda kwambiri moti sizingayerenso. Chitsanzo: Malaya anga athimbirira. (b) Kusaoneka bwino chifukwa cha mavuto. Chitsanzo: Mkazi wakwatiwa sabata yatha uja wathimbirira kale. Kuthimbwidzika: Kuyenda moyerekedwa. Chitsanzo: Akumayenda mothimbwidzika ngati wamva zoti pali amene akumufuna. Kuthira mā€™madzi momwe: Kuuza munthu nkhani yomwe akuidziwa kale. Chitsanzo: Nkhaniyo inapheduka chifukwa atakumana ndi mnzakeyo anamuuza zonse. Samadziwa kuti 198