Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 197

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: (1) Mwana akatha msinkhu amayamba kuvuta. (2) Mwana asanathe msinkhu mumafunika kumulangiza kuti asadzadabwe thupi lake likayamba kusintha. Kutha psiti: Kutheratu, kufa onse. Chitsanzo: Atsikana onse othamanga anatha psiti. Kutha thupi: Kuwonda. Chitsanzo: Pamene mwanayu akukulamu wayamba kutha thupi. Kuthamanga magazi: Kupupuluma, kusaugwira mtima. Chitsanzo: Mayi musathamange magazi, tikupatsani! Kuthamanga mwazi: Kupupuluma, kusaugwira mtima. Chitsanzo: Mayi musathamange mwazi, tikupatsani! Kuthamangathamanga: Kugwira ntchito kapena kuchita bizinezi kuti upeze kenakake. Chitsanzo: Ndikapanda kuthamangathamanga ndidya chi- yani m’tauni muno? Kuthamangitsa: (a) Kuuza munthu kuti achoke. Chitsanzo: Ana awo aja anawathamangitsa pakhomo. (b) Kuthamanga kuti ugwire munthu kapena kumupiri- kitsa. Chitsanzo: Akuthamangitsa galu. Kuthamangitsa: Kuuza munthu kuti achoke pakhomo. Angatanthauzenso kutsatira munthu amene akuthawa pomuthamangitsa. Chitsanzo: Anawathamangitsa palendi chifukwa sankali- pira. Kuthambitsa: Kukhaulitsa. Chitsanzo: Amuthambitsa anzake odziwa zigogodo. Kuthambitsa: Kukhaulitsa. Chitsanzo: Manoma athambitsa Siliva ndi zigoli ziwiri kwa du. 196