Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 196
Paphata pa Chichewa
(c) Kumwa.
Chitsanzo: Tiyeni tikatchaye tiyi.
Kutchetcherera: Kukopa mkazi kapena mwamuna kuti
ugone naye. Amayerekezera zimene tambala amachita ak-
amafuna thadzi.
Chitsanzo: Anyamatawa akumatchetcherera atsikana.
Kutchukuma: Kuvutika kugwira ntchito kapena kugulitsa
kanthu koma osapeza ndalama.
Chitsanzo: Malonda avuta patauni pano, ukumatha
kutchukuma tsiku lonse, osapeza olo 1 tambala.
Kuteketa (tekedza): Kudya.
Chitsanzo: Chichokere m’mawa akungoteketa makaka.
Kutemberera: Kunenera zoipa kuti zidzamuchitikire.
Chitsanzo: Umphawiwutu anakutembererani agogo anu!
Kutenderera: Kukometsera.
Chitsanzo: Nkhani yake ija anaitenderera kwambiri moti
imangokhala ngati yabodza.
Kutenga mtima:
(a) Kukopa.
Chitsanzo: Ndalama zija ndi zimene zinanditenga mtima.
(b) Kupweteketsa mtima.
Chitsanzo: Mawu ananena aja ananditenga mtima.
Kutenga zosatenga: Kutenga matenda.
Chitsanzo: Ndamva kuti ukuyenda ndi mtsikana wotakata
uja, samala utenga zosatenga.
Kutengeka: Kukopeka ndi chinthu.
Chitsanzo: Mwanayu ndi wotengeka.
Kutha mawu: Kuyankhula kwambiri, kulalata.
Chitsanzo: Ukakhala walungalunga osamatha mawu,
chilemba chimachita kubwera.
Kutha msinkhu: Kukula, kuyamba kusamba kapena
kutulutsa umuna.
195