Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 195
Paphata pa Chichewa
Kutasa: Kuchita zinthu moyerekedwa, kuchita zinthu
momasuka kwambiri, kukomedwa.
Chitsanzo: Mmene achokamu mpamene wantchito uja
watasa.
Kutaya bomwetamweta: Kutaya mwayi wopezapeza.
Chitsanzo: Munakana zoona! Apa ndiye mwataya bomwe-
tamweta.
Kutaya madzi: Kukodza.
Chitsanzo: Ndidikireni nditayeko madzi paselipa.
Kutaya mimba: Kupha mwana wosabadwa.
Chitsanzo: Boma likulola azimayi omwe atenga mimba
zosakonzekera kuti azitaya mimba.
Kutaya mtima: Kuyamba kuona kuti zinthu sizingayen-
denso, sizingasinthe.
Chitsanzo: Ndinataya mtima nditaona kuti zaka zikudutsa
asakuimba foni.
Kutaya nthawi: Kuononga nthawi.
Chitsanzo: Mukungotaya nthawi yanu kulimbana ndi ine.
Kutayira kamtengo: Kupereka ulemu.
Chitsanzo: Ndawataira kamtengo, akanakhala ena sa-
kanaugwira mtima!
Kutchalitchi: Mawu amene amanenedwa ponena za
kusukulu, popeza masukulu ambiri akale anali a
tchalitchi.
Chitsanzo: Ifetu kutchalitchi sitinapiteko, moti sitidziwa
kuwerenga.
Kutchatchatuka: Kuchenjeretsa.
Chitsanzo: Mwana ameneyu ndi otchatchatuka.
Kutchaya: Kumenya.
(a) Chitsanzo: Mtsikana ameneyu ndimutchaya.
(b) Kuimba, kukoka chingwe.
Chitsanzo: Tiwatchayire lamya.
194