Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 194
Paphata pa Chichewa
Kusweka mutu: Kukhala wolongolola, wovuta.
Chitsanzo: Ntchito ngati zimenezi zimafuna anthu osweka
mitu.
Kutafula: Kulalata.
Chitsanzo: Akayamba kutafula mungochokapo.
Kutafuna mlandu: Kuyankhula pamlandu.
Chitsanzo: Anthuwo atasonkhana, amfumu anayamba
kuutafuna mlanduwo.
Kutakataka: Kugwira ntchito, kuchita khama.
Chitsanzo: Mkazi amafunika azikhala wotakataka.
Kutalitali: Kulephereratu. Anganenedwenso potanthauza
kuti si zoona ngakhale pang’ono.
Chitsanzo: Kodi anapezadi zimene ankafuna? Kutalitali!
Kutama (kutamanda): Kulemekeza.
Chitsanzo: Ndi omwewo amene amakutamani, ine ayi. (2)
Akuona ngati ndidziwatamanda!
Kutambalala:
(a) Kukhazikika.
Chitsanzo: Musabweretu kudzatambalala pakhomo pano.
(b) Kukhala moongola miyendo.
Chitsanzo: Uli tambalale apa, m’malo moti uzikagwira
ntchito uko! (2) Mwamuna sakhala motambalala.
Kutamidwa: Kulemekezedwa.
Chitsanzo: Amakutamani ndi akazi anu omwe aja, ine ayi!
Kutantha: Kunena zina.
Chitsanzo: Fotokoza bwinobwino iwe, osamangotantha.
Kutapa m’kamwa: Kubwera kudzakufunsa kapena kud-
zayankhula nawe kuti akutole zifukwa.
Chitsanzo: Anabwera kuno kudzanditapa m’kamwa.
Kutapakutaya: Zambirimbiri.
Chitsanzo: Ndalama ife ndi kutapakutaya.
193