Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 192
Paphata pa Chichewa
Kusowa mtengo wogwira: Kusowa chochita.
Chitsanzo: Si bwino kumasekana pamavuto chifukwa na-
wenso pamawa, ukhoza kudzasowa mtengo wogwira.
Kusudzula: Kuuza munthu kuti azipita kwawo banja
likatha. Nthawi zina anthu amawapatsa ndalama mwina 2
kwacha monga malipiro achipongwe osonyeza kuti
awasudzula.
Chitsanzo: (1) Pano sali pabanja, anawasudzula akazi
awo. (2) Ingondisudzulani ngati simukundifuna,
mwamuna si inu nokha padzikoli!
Kusula:
(a) Kufunira munthu mankhwala obereketsa.
Chitsanzo: Ataona kuti zavuta, anapita kukasulitsa
mankhwala.
(b) Kuthandiza kuti ukhale wanzeru.
Chitsanzo: Aphunzitsi a m’Malawi muno amasula ana
okalowa m’sukulu za ukachenjede. Koma iwowo sasintha-
yi. Amadzamwalira akukongolabe katapira.
(c) Kupanga khasu kapena nkhwangwa. Zinthu zimene
zimasulidwa zimakhala zachitsulo.
Chitsanzo: Bambo anga amasula makasu.
Kusunga chakukhosi: Kusunga chifukwa, kudana ndi
munthu chifukwa cha zimene anakuchitira.
Chitsanzo: Anthu amasangalala m’banja akamapanda
kusungirana chakukhosi.
Kusunga nthawi: Kubwera pa nthawi yake, kusachedwa.
Chitsanzo: (1) Mabwana a pano sasunga nthawi. (2) Ali-
yense azolowere kumasunga nthawi.
Kusunsunuka: Kukula.
Chitsanzo: Mwanayutu wasunsunuka, mpofunika mumu-
patse malangizo.
Kusupa (kufupa): Kupereka mphoto.
Chitsanzo: Sindingasupe gule wosavinga bwino ngati
ameneyu!
191