Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 191
Paphata pa Chichewa
Kusoloka: Kutheratu kwa nyama kapena zomera.
Chitsanzo: Mitundu yambiri ya nsomba inasoloka.
Kusololoka: (1) Kukula mofulumira, kutalika.
Chitsanzo Ana a masiku ano akumangosololokera
m’mwamba. (2) Koma ndiye wasololokatu, mpaka kundi-
posa msinkhu?
Kusomeka:
(a) Kuika munthu malo ena, kaya paudindo.
Chitsanzo: Boma linadzatisomeka kumudzi kuno.
(b) Kuzika mtengo kapena chinthu penapake.
Chitsanzo: Someka mtengowu kutsindwiko.
Kusongola:
(a) Kudula chinthu kuti chisongoke, chikhale chobaya,
mwachitsanzo kusongola pensulo.
Chitsanzo: Akazi ambiri ali ndi milomo yokhala ngati
achita kusongola.
(b) Kukhala m’galimoto koma n’kutulutsa chigongono
panja.
Chitsanzo: Anzanu mkono wawo unapita chifukwa
chokonda kusongola akakwera galimoto.
(c) Kukhala pansi mosonyeza kuti ukumva bwino.
Chitsanzo: Ndinakuonani mutasongola panjinga.
Kusonkhezera: Kulimbiktsa.
Chitsanzo: (1) Kumene mukuchitakutu ndi kusonkhezera
mavuto! (2) Si bwino kumasonkhezera kuti anzako
amenyane.
Kusosa: Kudumpha tsiku limodzi. Nthawi zina amatan-
thauzanso kuchotsa ntchire m’munda pokonzekera ku-
limanso mbewu zina.
Chitsanzo: Tingososa mawali, tidzapita mkucha.
Kusosoka mthenga: kupusa.
Chitsanzo: Munthu woyerekedwa amafunika kumusosola
mthenga.
190