Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 19

Paphata pa Chichewa Bongobongo: Ubongo. Chitsanzo: Amachita zinthu ngati alibe bongobongo. Bongwe: Mwana wasukulu yemwe wangobwera kumene makamaka amene ali makalasi oyambirira. M’buyomo anthu amenewa ndi amene ankazunzidwa akafika pasukulu. Mawuwa angatanthauzenso munthu wosadziwa zinthu. Chitsanzo: Nafenso tinazunzika chonchi tili mabongwe. Bopha: Kuvala. Chitsanzo: Wabopha suti. Bowa bwanga: Kuchedwa, kuchita zinthu mwachidodo. Chitsanzo: Osamachita za ubowa bwanga. Bububu: Munthu wosayankhula. Chitsanzo: Akungokhala ngati bububu. Bulutu: Munthu wopusa. Chitsanzo: Mnzanu uja ndi bulutu. Buluzi: Wopanda ntchito, wopanda nzeru. Chitsanzo: Ndiwe buluzi eti! Buma maliro: Kulira koyambirira pamaliro. Chitsanzo: Tabwera titamva kubuma. Bunobuno: Ali wosavala. Chitsanzo: Wamisala uja akumayenda ali bunobuno. Bunobwamuswe: Ali wosavala. Chitsanzo: (1) Mmene anthu akuvalira masiku ano n’chimodzimodzi kuyenda bunobwamuswe. (2) Akumazungulira nyumba ali bunobwamuswe. Buntha pakamwa: Kulephera kuyankhula bwino. Chitsanzo: Mose anali munthu wobuntha pakamwa. 18