Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 189

Paphata pa Chichewa ndikudabwa kuti tikusekananso zikundu! Kuseleulana: Kunenana chipongwe. Chitsanzo: Ndimaseleulana ndi alamu anga. Kusemphana chichewa: Kuyambana, kusagwirizana. Chitsanzo: Anthu aja anasemphana chichewa. Kusemphana chichewa: Kuyambana. Chitsanzo: Mabwana anthu asemphana chichewa. Kusemphana maganizo: Kusagwirizana pa nkhani ina- yake. Chitsanzo: Asiya kuyankhulana chifukwa asemphana ma- ganizo. Kusenza katundu wako: Aliyense adzalimbana ndi mavuto ake. Chitsanzo: Zinthu zikavuta aliyense amasenza katundu wake. Kusesa mudzi: Kuchita mankhwala kuti mfiti zonse zi- choke. Mawuwa amanenedwa chifukwa cha zikhulupiriro zoti munthu amatha kuchita mankhwala kuti mnzake afe. Chitsanzo: Kubwera ng’anga kuti idzasese mudzi. Kusetekera: Kunyambitira. Chitsanzo: Ukamasetekera m’manja suzidya ndi ine! Kuseweretsa ndalama: Kugwiritsa ntchito ndalama mosasamala. Chitsanzo: Amuna anu achoka osasiya ndalama yandiwo aja akuseweretsa ndalama m’taunimu. Kuseweretsa ndalama: Kugwiritsira ntchito ndalama mo- sasamala. Chitsanzo: Ankaseweretsa ndalama, pano zamuthera ndipo maluzi amukamata. Kushupa: Kuvuta, kusautsa. Chitsanzo: (1) Abwana anga amandishupa kwabasi. 188