Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 188
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Atsikana ambiri amene amapita kuchinamwali,
amachita mwambo wa kusasa fumbi.
Kusasa: Kukana munthu, kusiya kucheza naye.
Chitsanzo: Kodi anzanu aja anakusasani?
Kusasantha: kumenya modetsa nkhawa.
Chitsanzo: Akakugwiratu akusasantha.
Kusasatuka: Kutengeka kwambiri.
Chitsanzo: Ndani angafunsire mtsikana wosasatuka ngati
ameneyu!
Kusatha phazi: Kusasiya kupita kwinakwake.
Chitsanzo: Satha phazi pakhomo pano.
Kusationa tulo: Kusagona.
Chitsanzo: Dzulo sindinatione tulo, ndimamva kutentha
ngati ndili m’bokosi.
Kusavuka: Kuonekera poyera, kupusa.
Chitsanzo: Khalidwe lanuli musavuka nalo!
Kusefukira:
(a) Kudzadza kwambiri kwa madzi.
Chitsanzo: Katundu wawo anapita ndi madzi osefukira.
(b) Kuyankhula mosaganiza bwino.
Chitsanzo: Nthawi zambiri amayankhula mosefukira.
(c) Kutayikira.
Chitsanzo: Thobwa likusefukira m’kapu.
Kuseka chikhakhali (chikhakhade): Kuseka kwambiri.
Chitsanzo: Ukayankhula zopanda mnzeru amakuseka
chikhakhali.
Kusekana zikundu: Kunyozana mavuto omwe nonse muli
nawo.
Chitsanzo: Tisamasekane zikundu eti! Musaiwaletu kuti
nanunso khalidwe lanu ndi lomweli.
Kusekana zikundu: Kuseka mavuto omwe nonse muli
nawo.
Chitsanzo: Tonse ndi akuda ngati makala, ndiye
187