Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 186

Paphata pa Chichewa Kusalowa m’nyumba: Kusagonana ndi mkazi kapena mwamuna wako. Chitsanzo: Akazi awo amadandaula kuti amuna awo salowa m’nyumba pomwe amagona momwemo. Kusamba zitsulo: Mawu amenewa amanenedwa ngati munthu wachedwa kwambiri kubafa. Pokokomeza amanena kuti wachedwa chifukwa m’malo mosamba madzi, amasamba zitsulo. Chitsanzo: Kodi kubafako mukusamba zitsulo? Kusamba: (a) Munthu amene ali nazo zambiri ndipo zina aman- goseweretsa. Chitsanzo: Anzathutu mukusamba m’ndalama! (b) Matenda amene azimayi amadwala mwezi ndi mwezi. Chitsanzo: Mtsikana akamangolusa popanda chifukwa, amakhala kuti akusamba. Kusambira m’manja: (a) Kugwira ntchito mwaluso zedi. Chitsanzo: Nyumbayo anaimanga moisambira m’manja. (b) Kuchita zinazake kuti pamapeto pake usadzakhale ndi mlandu, kunyanyalira. Chitsanzo: Katundu wanu ndi uyu, zikakuvutani mu- sabwere, ndakusambirani m’manja. Kusambira m’ndalama: Kukhala ndi ndalama zochuluka kwambiri. Chitsanzo: Azibusa ambiri akusambira m’ndalama chifu- kwa chochita bizinezi yoopseza anthu ndi Gehena. Kusambitsa ndi zibakera: Kumumenya koopsa. Chitsanzo: Mwanayo anawasambitsa bambo ake ndi zibakera. Kusambuka: Kunyozeka, kuvutika. Chitsanzo: (1) Akutinyoza chifukwa tasambuka. (2) Anzanu aja andisambula. 185