Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Página 184

Paphata pa Chichewa (b) Kusaphedwa kapena kusakumana ndi tsoka linalake. Chitsanzo: Anapulumuka pa ngozi yoopsa. (c) Kuchitika mwangozi kapena mwadzidzidzi. Chitsanzo: Chiphwisi chinandipulumuka. Kupumuntha: Kumenya munthu mwankhanza. Chitsanzo: Akakupeza ukuchita zimenezo akupumuntha. Kupunduka: Kukhala ndi chilema. Chitsanzo: Ali ndi ana awiri opunduka. Kupungula mpweya: Mawu amene eni nyumba amauza mlendo akamafuna kumuuza kuti anene chimene wabw- erera. Chitsanzo: Tati tikupunguleni mpweya! Kupunthwa: Kulakwitsa chinachake. Chitsanzo: Munthu aliyense amapunthwa nthawi zina. Kuputa mavuto: Kuyamba dala zinthu zomwe zikhoza kukuika m’mavuto. Chitsanzo: (1) Anawa andiputira mavuto. (2) Amenewatu akuwaputa mavuto, aziona! Kupuwala: Kukhala ndi chilema. Chitsanzo: Amalume awo ndi opuwala. Kupwaira: Kugwira mwankhanza. Chitsanzo: Atsamunda anapwaira anthu onse omwe ankalimbana nawo. Kupwintha: Kuika zambiri, kuwonjezeza zambiri. Chitsanzo: (1) Mu ndiwozi apwinthamo mchere wambiri. (2) N’chifukwa chiyani mwapwintha ufa wambiri chonchi? Kupyolera: Kudzera. Chitsanzo: Amatumiza zinthu kupyolera pabasi. Kupyontha: Kumwa, kuyamba, kutsopa. Chitsanzo: Ndinawapeza akupyontha kabotolo ka mame. 183