Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 183

Paphata pa Chichewa Kupsa: Kukhala opanda ndalama. Chitsanzo: Pano ndiye ndapseratu. Kupsipsintha: (a) Kutsopa bwinobwino. Chitsanzo: Atamaliza kudya anayamba kupsipsintha ma- fupa. (b) Kuonda kwambiri. Chitsanzo: Anzawo onenepa aja anapsipsinthika. Kupsopsona: Kukisa. Chitsanzo: Akufuna akupsopsone. Kupuka: Kusupuka, kuchoka khungu. Chitsanzo: Anapsa ndi madzi otentha moti wakupukiratu. Kupukusa mutu wopanda nyanga: Kudzimvera chisoni, kudandaula. Chitsanzo: Ndikaganizira mavuto amene ndikukumana nawo, ndimangopukusa mutu pukupuku. Kupukusika: Kuyenda moyerekedwa. Chitsanzo: Akamadutsa apa akumachita kupukusika. Kupululitsa: (a) Kulepheretsa, kupusitsa. Chitsanzo: Anzanu aja andipululitsa. Eti amadutsa ine ndikufuna kuba magwafa! (b) Kuchititsa wina kuti apulule zinthu. Chitsanzo: Apululitsa mango onse aja. Kupululuka: (a) Kufa ambiri. Chitsanzo: (1) Anthu ambiri apululuka chifukwa cha njala. (2) Edzi ikupulula miyoyo ya anthu. (b) Kuthothoka. Chitsanzo: Mango onse apululuka. Kupulumuka: (a) Kutsomphoka kapena kugwa kuchoka m’manja. Chitsanzo: Poto anandipulumuka. 182