Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 18

Paphata pa Chichewa yomweyo mnzake wina ananena kuti “bowa wanga!” Chifukwa cha chidodo mnzakeyo anazula bowayo pomwe anali woyambirira kumuona ndi iyeyo. Chitsanzo: Malonda a mtedza samafuna munthu wa bobobo. Bodza lofuka utsi: Bodza lalikulu. Chitsanzo: Ndinadziwiratu kuti limeneli ndi bodza lofuka utsi. Bola moyo: Mawu amene amanenedwa m’malo monena kuti, nanga titani. Mawuwa amanenedwa ukamachita zinthu mokakamizika. Chitsanzo: Tidyabe zomwezi, bola moyo. Bola: (a) Mawuwa amanenedwa munthu akamanena kuti zili bwinobe koma osati kwenikweni. Chitsanzo: Bola atipatsa poyambira, kusiyana ndi kungokhaliratu. (b) Kampukutu ka chamba. Chitsanzo: Amugwira ndi kabola ka chamba. Bomba: (a) Mkazi wokongola. Chitsanzo: Mwana wa mayiwa ndi bomba. (b) Kusiirira zinthu zomwe zikhoza kudzabweretsa mavuto aakulu m’tsogolo. Chitsanzo: Matenda akubisawa ndi bomba, akadzaphulika tidzadziwa. Bombono: Bondo. Chitsanzo: Waguluka bombono. 17