Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 179

Paphata pa Chichewa Kuphuvumula: Kumenya munthu modetsa nkhawa. Chitsanzo: Anzake ndi amene amuphuvumula. Kuphwa madzi: Kupumula kapena kupuma kugwira ntchito inayake. Chitsanzo: Nthawi yotentha ino umafunika kupita kunyanja n’kukaphwa madzi. Kuphwanya kwa thupi: Kumva kupweteka m’thupi chifu- kwa cha matenda kapena chifukwa chogwira ntchito yole- metsa. Chitsanzo: Thupi langa likamaphwanya, malungo ama- khala akundizemberera. Kuphwanya malamulo: Kuchita zinthu zosemphana ndi malamulo. Chitsanzo: Anthu onse amene akuphwanya malamulo amangidwa. Kuphweka: Kusavuta. Chitsanzo: Kuyendetsa galimoto ndi kophweka. Kuphyontha (kupyontha): Kutsopa, kumwa. Chitsanzo: Ndinamupeza akuphyontha zakumwa zozi- ziritsa kukhosi. Kupikula: Kugula zinthu zambiri nthawi imodzi. Chitsanzo: Ndikupita kukapikula katundu. Kupima: (a) Kuzolowera mavuto. Chitsanzo: Ine ndinapima ndi mavuto. (b) Kusapsa. Chitsanzo: Chimanga chimene amakazinga chija chapima. Kupinda: Kusokoneza munthu kuti asamve zimene mukunena. Chitsanzo: Koma ndiye mwatipindatu, mukutanthauza chiyani? 178