Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 178

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: M’munda analima chimanga muja aphinziramo mbatata. Kuphipha: Kugwedezekagwedezeka kapena kuti kuthatha komwe kumachitika munthu kapena nyama zina zikatsa- la pang’ono kufa kapenanso zikapanikizika. Chitsanzo: (1) Nsombayo inayamba kuphipha ataiponyera pamtunda. (2) Aliyense anayamba kulira munthuyo atayamba kuphipha. Kuphofomoka: Kugwa modetsa nkhawa. Chitsanzo: Mwana wanu waphofomoka mumtengo. Kuphotchora: Kusiya mkazi kapena mwamuna wako n’kukagona ndi wina. Chitsanzo: Mwamunayu anaphotchora. Kuphuka: Kuchira. Chitsanzo: Achibale onse omwe amafuna kulanda chuma, sanasangalale ataona kuti m’bale wawo waphuka. Kuphula: (a) Kuchiritsa munthu nthenda imene yakanika asing’anga ena. Chitsanzo: Amene uja amadwala mwakayakaya, kaya ndi ndani wamuphula? (b) Kulemera, kupeza ndalama zambiri. Chitsanzo: Anthu onse omwe ndinayamba nawo bizinezi anaphula. Kuphuluza: Kulakwitsa, kusaponda kapena kugwira bwino. Chitsanzo: Anamuchotsa ntchito ataphuluza n’kuyamba- na ndi abwana. Kuphuluza: Kuteleleka, kulakwitsa, kuponda kapena kugwira molakwika. Chitsanzo: Ndinaphuluza n’kubinya phazi. Kuphupha: Kudzimenyetsamenyetsa. Chitsanzo: Khukuyo ataidula mutu inayamba kuphupha. 177