Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 177
Paphata pa Chichewa
Kupheduka: Kuululika.
Chitsanzo: (1) Muyaluka nkhaniyi ikapheduka. (2) Ndani
amene waphedula nkhaniyi?
Kuphera mphongo: Kutsirira ndemanga, kusonyeza kuti
ukugwirizana ndi zimene wina wanena.
Chitsanzo: Ndikufuna kuphera mphongo pa mawu amene
akuluwo anena.
Kuphera ufulu: Kulakwira munthu posalemekeza ufulu
wake.
Chitsanzo: Ana a masiku ano ukamawauza kuti asamava-
le ngati akupita kubafa, akumakuyankha kutu
usawaphere ufulu.
Kuphetsa:
(a) Kugulitsa.
Chitsanzo: Ndaphetsa njinga yanga ija.
(b) Kupweteketsa munthu wina, kuchititsa kuti wina
aphedwe.
Chitsanzo: Zimene mukuchitazi muwaphetsatu akazi anu
aja.
Kuphikana (kuphika): Kumenyana, kumenya munthu.
Chitsanzo: (1) Ndinawapeza akuphikana. (2) Anzake
amuphika.
Kuphikitsa thobwa: M’madera a m’chigawo chapakati,
amati akaphika thobwa, amadzaliwiritsanso kachiwiri.
Zimene amachitazi amati kuphikitsa thobwa.
Chitsanzo: Kodi mwaphikitsa thobwali?
Kuphimba m’maso: Kupusitsa, kunamiza, kunyenga.
Chitsanzo: Akungofuna kutiphimba m’maso.
Kuphinza: Kuvala.
Chitanzo: Koma ndiye waphinza kasuti kabwinotu!
Kuphinzira mbatata: Kulimba mtumbira n’kudzalapo
mbatata.
176