Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 176
Paphata pa Chichewa
Kupereseka: Kuvutika koopsa, kutha, kukhulika.
Chitsanzo: Mavutowa akamatisiya tikhala titapereseka.
Kupeza mpumulo: Mawu amenewa amabwera
tikamanena za munthu amene anali pamavuto ndiye
mavutowo atha kapena munthu amene wakhala nthawi
yaitali osapeza banja kenako n’kulipeza.
Chitsanzo: (1) Ndipite kumudzi kuti mwina ndikapezeko
mpumulo. (2) Musiyeni akwatiwe kuti nayenso apeze mpu-
mulo.
Kupha mwambi: Kunena mwambi.
Chitsanzo: Akamayankhula amakonda kupha miyambi.
Kupha nyerere: Kuyenda wapansi.
Chitsanzo: (1) Ana a mabwana savutika n’kumapha nyere-
re mumsewumu. (2) Ndaganiza zogula njinga, ndatopa ndi
kupha nyerere.
Kupha ulusi: Kuvala bwino, kutchena.
Chitsanzo: Koma ndiye mwapha ulusitu anzathu!
Kupha: Sasatitsa, kapena zoloweretsa ana zoipa
pomangowachitira zimene akufuna.
Chitsanzo: Anawatu munawapha, adzavutika muk-
adzamwalira.
Kuphana maso: Maso kuyang’anizana.
Chitsanzo: (1) Anachita manyazi titaphana maso. (2) Aku-
nama kuti sanandione pomwe tinaphana maso.
Kuphanda: Kuwerenga.
Chitsanzo: Ndinamupeza akuphanda.
Kuphangira: Kutenga zambiri.
Chitsanzo: Tikamagawana akumakonda kuphangira.
Ulendo uno ndichita zandekha.
Kuphaphalitsa ndi mafunso: Kupanikiza ndi mafunso.
Chitsanzo: Nanunso anakuphaphalitsani ndi mafunso?
175