Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 174

Paphata pa Chichewa Kupachika: Kuika wina pamavuto. Chitsanzo: Pamenepatu ndiye mwandipachika! Zoona mwawauzanso zimenezi! Kupaka chipere: Namizira. Chitsanzo: Ndikuona kuti anangomupaka chipere. Kupaka: Kunena kuti walakwa koma asali iyeyo. Chitsanzo: Mimbayi si yake, angomupaka. Kupala pakamwa (m’kamwa): Kukuyamba. Chitsanzo: (1) Akungofuna kundipala pakamwa. (2) Anabwera n’cholinga choti adzangondipala m’kamwa. Kupala pakamwa: Kubwera kudzakufunsa kapena kudza- yankhula nawe kuti akutole zifukwa. Angatanthauzenso kubwera kudzakuyamba. Chitsanzo: Samabwera kudzacheza, anabwera kudzandi- pala pakamwa. Kupala: (a) Kulephera. Chitsanzo: Mdani wako akamapala umafunika ungomusi- ya kuti amalizitse. (b) Kuchotsa zimene zili pamwamba pa chinachake pog- wiritsa ntchito chopalira. Chitsanzo: Akupala mtengo. (c) Kutenga moto n’kupita nawo kwina kuti ukaukoleze. Chitsanzo: Ndimakapala moto. (d) Kuputa kapena kuyamba munthu. Chitsanzo: Amabwera kuti adzandipale mkamwa. Kupalamula: Kulakwa, kuyambana ndi wina. Chitsanzo: (1) Amene atabwere mochedwa wapalamula! (2) Nkhope zina zimangooneka zopalamula kale chifukwa cha mavuto. Kupalapatika: Kungovutika pachabe. Chitsanzo: Palibe chimene angachite ngakhale titapalapatika bwanji? 173