Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 172
Paphata pa Chichewa
Kuona m’magonero: Kudziwa mmene ulili.
Chitsanzo: Osamangoitana aliyense kuti abwere kwanu
angadzakuone m’magonero n’kukubera.
Kuona m’mimba: Kuyang’ana mwamwano.
Chitsanzo: Musandiyang’ane ngati mukundiona m’mimba.
Kuona manthu wamavuto: Kukumana ndi mavuto aaku-
lu kwambiri, mavuto osaneneka.
Chitsanzo: Chaka chino ndiona manthu wamavuto.
Kuona ndi diso limodzi: Nyoza.
Chitsanzo: Anzake amangowaona ndi diso limodzi.
Kuona ng’ala: Kusaona bwino.
Chitsanzo: Munaona ng’ala, si mango ndi mapapaya.
Kuona ngati wavula: Kukuyang’ana monyoza kapena
kukuona ngati munthu wopusa.
Chitsanzo: Anzakefe amangotiona ngati tavula.
Kuona patali: Kuganizira zotsatira za zimene ukuchita
kapena kuganizira za m’tsogolo.
Chitsanzo: Pulezidentiyu amaona patali.
Kuona zilubwelubwe: Kusokonezeka, kuona zinthu zosi-
yana kwambiri ndi zimene zilipo.
Chitsanzo: Nanunso mwayamba kuona zilubwelubwe.
Kuoneka bo: Mawu amene achinyamata amanena
poyamikira munthu kuti akuoneka bwino.
Chitsanzo: Msungwana, ukuoneka bo!
Kuoneka ngati kamvuluvulu: Kuvala zovala zosaoneka
bwino, kuvala nsanza.
Chitsanzo: Kutchena konsekuja, makolo awo amangoon-
eka ngati kamvuluvulu!
171