Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 17
Paphata pa Chichewa
Bibida: Mowa.
Chitsanzo: Bibida ndi amene amawalowa m’thumba, moti
akapeza ndalama pakhomo pano pamawayabwa.
Bingiza: Chimpopamanyi.
Chitsanzo: Akufuna aitanitse chibingiza.
Birimankhwe (tonkhwetonkwe): Munthu wosinthasitha.
Chitsanzo: Amene uja ndi birimankhwe (tonkhwetonkhwe).
Akangochoka kutchalitchi amavula Chikhirisitu
n’kuchisiya apo, kenako amavala usatana.
Biriwira: Kukhala ndi thanzi, kunenepa.
Chitsanzo: Chaka chino tibiriwira, chakudya ndi kutapa
kutaya.
Bisa nkhope: Kukhala ngati sukuona.
Chitsanzo: Osamabisa nkhope ukakumana ndi wachibale.
Bisala pachipande: Kunama
Chitsanzo: Ameneyu akubisala pachipande.
Bisira kampeni kumphasa: Kuchitira munthu chiwembu.
Chitsanzo: Ndimadziwa kuti amandibisira kampeni
kumphasa.
Bizinezi yotentha: Bizinezi yobweretsa ndalama zambiri.
Chitsanzo: Akuchita bizinezi yotentha.
Bobobo: Kuchedwachedwa, chidodo. Mawuwa anachokera
pa kankhani kena konena za munthu wachibwibwi yemwe
anapita ndi anzake kukazula bowa. Ndiye mukamayenda
gulu, munthu amene wayambirira kuona bowa amafunika
kunena mokweza kuti “bowa wanga!” kuti anzake adziwe
kuti wayambirira kuona bowayo ndi iyeyo. Ndiye
wachibwibwi uja ankangoti bo bo bo, osamalizitsa. Nthawi
16