Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 169

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Atanena zimenezi anangonyanyula gulu la anthulo moti amafuna kumumenya. Kunyeka: (a) Kukolera moto. Chitsanzo: Makalawa anyeka. (b) Kupanga madzi. Chitsanzo: Pansi pa mtsuko paja payamba kunyeka madzi. Kunyema munthu: Anthu amene amasewera mpira amanena mawu amenewa munthu wina akaponda mnzake. Chitsanzo: Anamutulutsa chifukwa ananyema mnzake. Kunyenya: (a) Kugwira ntchito mwaulesi. Chitsanzo: Akabwera kuntchito kuno amangonyenya. (b) Kuphwanya chithu kuti chikhale tizidutsa ting’onoting’ono. Chitsanzo: Ndani wanyenya chigumuchi? Kunyenyerera: Kumwaza, ena amati kumbwezambweza zinthu monga shuga ndi zina. Chitsanzo: Ndani wanyenyerera m’nyumba ndakolopamu! Kunyepera: Kuzendewera galimoto, ngolo kapena chinthu china. Chitsanzo: Mwana wanuyu akumanyepera magalimoto. Kunyezimira: Kuwala. Chitsanzo: Golide amanyezimira. Kunyindirira: Kulimbikira kwambiri. Chitsanzo: Ukaona kuti mnzako akukuposa umafunika 168