Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 168
Paphata pa Chichewa
Kunkhuniza: Kuyankhula mobisa.
Chitsanzo: Mnyamata amene uja wandikunkhuniza.
Kunola mano: Kukonzekera kudya zankhuli.
Chitsanzo: Mpofunika tinole mano, tidyera nyama lero.
Kunong’a: Kukoma.
Chitsanzo: Kekeyu ndiye akunong’atu!
Kunong’oneza bondo: Kudzimvera chisoni kapena kud-
ziimba mlandu chifukwa cha zimene unasankha mo-
lakwika.
Chitsanzo: Anthu onse omwe sankalimbikira sukulu
amanong’oneza bondo.
Kunsakhuta: Kumanda.
Chitsanzo: Mbava ija tinakaikwirira kunsakhuta.
Kunsitu: Kumanda.
Chitsanzo: Masiku ano mitengo yatsala kunsitu kokha.
Kunyalanyaza: Kusafuna kuganizira zoipa zimene wina
wakuchitira, kusafuna kuchita zinazake.
Chitsanzo: (1) Anandilakwira koma ndinangosankha
kuinyalanyaza nkhaniyo. (2) Munthu ameneyu amakonda
kunyalanyaza pochita zinthu.
Kunyangala: Kuvuta, kuipa, kulusa.
Chitsanzo: (1) Agalu ake ndi onyangala. (2) Akazi awo aja
ndi wonyangala.
Kunyanyala: Kukwiya, kusiya kuchita zinazake.
Chitsanzo: Anyanyala chifukwa choti tawakaniza njinga.
Kunyanyula: Kuputa munthu, kuchititsa kuti munthu
akwiye.
167