Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 167
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Wangomanga kakhoma akaka basi, koma si
mtengo wanding’ambawo!
Kung’ombola maso: Kunyoza pomutulutsira munthu
maso.
Chitsanzo: Ataona kuti ndalephera ananding’ombolera
maso.
Kungogwera: Kungochita zinthu mwamwayi.
Chitsanzo: Anthu amene aja angogwera, sakanapambana.
Kungolota: Kugoganiza.
Chitsanzo: Kuti upeze yankho lolondola la samu umafu-
nika kuganiza, osati kungolota.
Kungwanjura: Kubera munthu.
Chitsanzo: Amugwanjura ndalama zonse.
Kuninkha: Kupatsa, kupereka.
Chitsanzo: (1) Musadandaule, nanunso akuninkhani zanu.
(2) Mukawatenga bwino akuninkhani makwacha.
Kunjanja:
(a) Kuyenda moyerekedwa.
Chitsanzo: Anyamata ambiri akamadutsa pagulu la atsi-
kana, amadutsa akunjanja.
(b) Kulephereka, kusatheka kwa chinthu.
Chitsanzo: Moni wakoyo wanjanja, ubwere udzapereke
wekha.
Kunjuta:
(a) Kugwada, kuwerama.
Chitsanzo: Mukamakayankhula ndi amfumu mukanjute.
(b) Kupita kuchimbudzi, kukabiba.
Chitsanzo: Mwana wanu wanjuta kuseriku.
166