Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 166

Paphata pa Chichewa Kunditola: Kundiderera, kundinyoza, kusiya kukule- mekeza. Chitsanzo: Ana a sukuluwa amanditola. Kundiwerenga: Kundilondalonda. Chitsanzo: Sindibwera pamayeso, chonde chepetsani kundiwerenga. Kundiyenda pansi: Kundipusitsa, kuchita zinthu mondibisila. Chitsanzo: Sikuti muzichita zinthu zondiyenda pansitu apa! Kundizolowera: Kusiya kuchita nane mantha, kusandilemekeza. Chitsanzo: Mwandizolowera eti? Kunena mosapita m’mbali: Kunena mwatchutchutchu, kunena mosazungulira. Chitsanzo: Ndinene mosapita m’mbali pano, ndinu opusa kwabasi. Kunena mosapsatira (kuyankhula mosapsatira): Kunena mosabisa mawu. Chitsanzo: Ukawafunsa, amangonena mosapsatira mawu. Kung’amba: (a) Kuthamanga kwambiri. Chitsanzo: Mwana ameneyu amang’amba. (b) Kudzera njira yachidule. Chitsanzo: Ndikuganiza kuti ndingong’amba ndi njira iyi kuti ndikafika msanga. Kung’ambidwa mtengo: Kuuzidwa kuti upereke ndalama zambiri pogula chinthu. 165