Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 165

Paphata pa Chichewa Kumwaza ndalama: Kugwiritsa ntchito ndalama mosasamala. Chitsanzo: Amuna anu achoka osasiya ndalama yandiwo aja akumwaza ndalama m’taunimu. Kumwera madzi: (a) Kugulitsa. Chitsanzo: Anali ndi nyumba koma anaimwera madzi. (b) Kuzisiya, kusaganizira kwambiri nkhani inayake. Chitsanzo: Nkhani ija ndangoimwera madzi, sindikufuna zoyambana nawo. Kumwera: (a) Kugwiritsa ntchito ndalama pogula mowa. Chitsanzo: Salale yonse wamwera. (b) Kumvetsa zinazake, kudziwa kwambiri zinazake. Chitsanzo: Masamuwa ndiye ndamwera, atabwera pa- mayeso sindingalephere. Kumwera: (a) Kumwa madzi utadya chakudya. Chitsanzo: Ndakhuta, tsopano ndimwere madzi. (b) Kudziwa zinthu, kuloweza zinthu. Chitsanzo: (1) Masamu amenewa ndinamwera. (2) Phunziro limeneli ndalimwera. Kundade: Munthu woyendayenda. Chitsanzo: Ukakhala kundade, zambiri zimakuphonya. Kundipatsa maganizo: Nkhani kapena chinthu chimene chingachititse kuti uziganiza kwambiri. Chitsanzo: Mwana ameneyu amandipatsa maganizo. 164