Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 164
Paphata pa Chichewa
Kumushisha: Kumuopseza.
Chitsanzo: Kunabwera anyamata enaake ndipo anayamba
kumushisha.
Kumutembenukira: Kumuukira, kusiya kugwirizana
naye.
Chitsanzo: Amene uja tsiku lina adzakutembenukirani.
Kumuwaza mchenga m’maso: Kumupusitsa.
Chitsanzo: Anachenjera anzake atamuwaza mchenga
m’maso.
Kumva bwino: Kusangalala. Angatanthauzenso kumva
kukoma.
Chitsanzo: Amamva bwino anzake akamavutika.
Kumva m’bebe:
(a) Kukhaulitsa.
Chitsanzo: Mumawanyoza asanabwere, ndiyetu mumva
m’bebe chifukwa akuchitani zoopsa.
(2) Kumva kutentha.
Chitsanzo: Ndiyandikireko motowu kuti ndizimva m’bebe.
Kumva mwala kupuma: Dziwa kuti pali kanthu kabwino.
Chitsanzo: Kodi galuyu akununkhidza pamenepa
chifukwa chiyani? Wamva mwala kupuma!
Kumvera m’maso: Kusamva.
Chitsanzo: Ndinakuuzanitu posachedwapa, kodi nanunso
mumamvera m’maso?
Kumwa inki: Kuphunzira.
Chitsanzo: Anthu amene anamwa inki savutikiratu.
Kumwaza maso: Kuyang’ana uku ndi uku.
Chitsanzo: Nditamwaza maso sindinawaone.
163