Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 163
Paphata pa Chichewa
Kumtima kwalira nkhwichi: Kuvutika mumtima.
Chitsanzo: Bwanayo anazindikira kuti kwabwera munthu
wina wamapepala abwino kuposa ake, kumtima kunalira
nkhwichi.
Kumtima mbee ngati waponda muufa: Kumva bwino
kwambiri utachita chinachake.
Chitsanzo: Kumtima kwake kuli mbee ngati waponda
muufa.
Kumudwala: Kufunitsitsa kuona munthu winawake.
Chitsanzo: (1) Mayi anga ndawadwala. (2) Ndabwera
chifukwa ndinakudwalani.
Kumudzala: Kulola munthu kukhazikika, kumunyen-
gerera.
Chitsanzo: Koma ndiye mukumudzalatu, abweranso mawa
muona!
Kumukonda mpaka aiwale kwawo: Kumukonda kwam-
biri kuti asalakelakenso zobwerera kwawo.
Chitsanzo: Uzimukonda kwambiri kuti aiwale kwawo.
Kumukuntha nayo ndodo (kumuphimba nayo ndodo):
Kumukwapula, kumumenya.
Chitsanzo: Mnzanu anabwera mochedwa uja amuphimba
nayo ndodo.
Kumumvetsa madzi: Kumukhaulitsa.
Chitsanzo: Amayerekedwa ndiye anzake anamumvetsa
madzi.
Kumupukwa: Kufunitsitsa kuona munthu winawake.
Chitsanzo: Makolo anga ndawapukwa.
162