Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 162

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Mwagwira ntchito kwabasi, kumeneko ndiye kukhala. Kumenyetsa nkhwangwa pamwala: Kukanitsitsa. Chitsanzo: Wamenyetsa nkhwangwa pamwala kuti sapitakonso. Kumera linunda: Kuyamba kudzimva, kuyamba kuyerekedwa, kudzikuza. Chitsanzo: Mmene awapatsa udindomu ayamba kumera linunda. Kumera mizu: Kukhazikika. Chitsanzo: Akamwini amayerekedwa akayamba kumera mizu pamudzi. Kumera nthenje: Kukhazikika. Chitsanzo: Chikondi chathu chamera nthenje. Kumeza: Kudya. Chitsanzo: (1) Ndinapita kukawaona ndipo ndinawapeza akumeza. (2) Tiyeni tikameze nsima. Kumkeka: Mkazi. Chitsanzo: Kodi a kumkeka ali bwanji? Kumoto: Kumaliseche. Chitsanzo: Anabuula atamumenya kumoto. Kumpando: Mawu omwe anthu amanena polemekeza munthu. Chitsanzo: Ali bwanji kumpando! Kumsitu: Kumanda. Chitsanzo: Anamupeza akuthyola mango kumsitu. 161